Wachiwiri kwa nduna yamaboma aang'ono, a Joyce Chitsulo, apempha mafumu kuti akhale patsogolo kulondoloza ntchito za chitukuko komanso ndalama zomwe boma likupereka kumadera ndicholinga choti masomphenya a chitukuko omwe mtsogoleri wadziko lino, Dr Lazarus Chakwera alinawo, atheke m’dziko mini.
A Chitsulo anena izi pa mwambo okweza GVH Matanda kukhala Sub Traditional Authority Matanda m’dera la Senior Chief Chitukula m’boma la Lilongwe.
Iwo ati boma lakhazikitsa ndondomeko monga za Mtukula Pakhomo, ndalama zakudera za Constituency Development Fund ngakhalenso zangongole, mwazina, choncho ndipofunika kuti mafumu adzionetsetsa kuti ndalama zikugwira ntchito zoyenera komanso kukagogoda m'makomo moyenera ngati anthu awo sakupindula.
Iwo atinso mafumuwa ali ndi udindo waukulu pogwirana manja ndi boma pothana ndi mchitidwe wa ziphuphu poonetsetsa kuti thandizo lomwe boma likupereka akuligawa kwa oyenera.
Mmawu ake, Senior Chief Kalumbu ati ntchito ya mafumu ndi kuthandizana ndi boma kubweretsa chitukuko, bata, mtendere komanso chilungamo choncho apempha mafumuwa kuti agwire ntchito limodzi ndi boma.