Mkhalakale pa ndale m’dziko muno, a Hilda Manjamkhosi, lero lachinayi pa 22 May 2025, anakacheza ndi wachiwiri kwa nduna ya maboma ang'ono omwenso ndi phungu wadera lakuzambwe m’boma la Mwanza, a Joyce Chitsulo, omwe adachita ngozi masiku apitawa.
Poyankhula ndi MBC munzinda wa Lilongwe, a Manjamkhosi omwe adakhalapo mkulu wa amayi ku chipani cha Malawi Congress (MCP) anati anachiona chanzeru kuti akawaone a Chitsulo ngati mbali imodzi yowalimbikitsa.
A Manjamkhosi anapita limodzi ndi mlangizi wa Prezidenti pa nkhani za amayi mchipani cha MCP, a Dorothy Chirambo.
Ndipo a Chitsulo ayamika anthu osiyanasiyana omwe akhala akumakawazonda.
Malinga ndi a Chitsulo, pali chiyembekezo kuti chikhakha chomwe adawaika adzachichotsa pa 2 June 2025, ndipo kwakukulu akuyamika Mulungu chifukwa cha zokoma zomwe wawachitira.