Psalu Psalu Sports
Ndi Mkoko pa Sports
#Kalliecesportswitness#
Tikulandileni madzulo a lero
Sunday pa 10 November 2024.
SPONSORED BY AGOGO A JOSHUA
Atsikana a Kabango Sisters afika mu finals ya Hon Joyce Chitsulo Netball Trophy.
Atsikana a Kabango akwapula Ilemba sisters ndi ma basket 38 kwa 25.
Zateremu Kabango Sisters yafika mu finals.
SPONSORED BY AGOGO A JOSHUA
Lero zalephereka kuti tidziwe oyamba kufika mu finals ya Hon Joyce Chitsulo 3.6 Million Kwacha Football trophy.
Ngakhale mpira unayamba mochedwa chifukwa cha ma player ena omwe amafuna kumenya mpira pomwe sanapange register, komabe
Mangulenje ndi Beato anatengetsana chulu cha tchula pomwe pa 90 minutes zatha 0 0. Ndipo zinalowa ku mapenalty pomwe tawona ma team onse akumenya ma penalty mwa ukadaulo. Onse kuchinya ma penalty 5 oyambilira 5 5, kenako inali yachimenye menye pomwe tawona onse akuchinya kukhala 6 6,
Malingana ndikuti kunayamba dima komiti inauza ref kuti basi apa zavuta tiyeni tidzakonzeso tsiku lina kuti okula ntima adzadziwike.
Kotero tidikila a komiti kuti atiuza zotani,
A Tambala aja anapanilirana, Atambwali akanadi kumetana lero, Patenga nyengo chiwonereni izi ma team kulepherana,
Funso mkumati kodi anamka kwa Sing'anga modzi? Kapena onse nsemba zawo kwa Chauta zinali zofanana?
Tiwona momwe zidzakhalire akamadzabwerezana.
Timva kuti malamulo amati chani zikatere ndikayankhula ine paja ndine wa mkamwa.
SPONSORED BY AGOGO A JOSHUA
Ilemba ndi a Katswili a Hurry 100 000 Bonanza yomwe imachitikila pa Ching'ombe.
Ilemba yakwapula Ng'onzo 1 zero chigoli chokhacho cha mkwerekwete. Chapatitsa sure Ilemba Stars.
Ndipo yomwe yakhala number 3 ndi Tinaliyani yomwe yaumbudza Kapherana pa ma penalty.
Kapherana ikupitilira kuyenda kuyipa akapanda kukonza zidzawavuta chaka cha mawa.
Sponsored by AGOGO A JOSHUA.
PSALU PSALU SPORTS DESK
Ikuti Happy Birthday Kwa Founder wa Psalu Psalu
Kalisto Sillia.
Psalu Psalu Team ikuti
HAPPY BIRTH DAY SIR.