Phungu wa kunyumba yamalamulo wadela la Mwanza West Constituency Hon Mai Joyce Chitsulo MP wati Mtsogoleri wadziko lino His Excellency the State President Dr Lazarus McCarthy Chakwera walemekeza anthu aku boma la Mwanza komanso anthu aku boma la Neno. Mai Chitsulo ati Mtsogoleri wadziko lino His Excellency Dr Lazarus McCarthy Chakwera wa walemekeza anthu amumaboma awiriwa pamene Mtsogoleri wadziko linonoyu wasankha kukhazikitsa dongosolo la logawa komanso kugulitsa zipanjizo za Ulimi zotsika mtengo (Launch of 2024/25 Affordable Inputs programme (AIP) kudelari . Mai Joyce Chitsulo athokonzanso Presidenti Chakwera kaamba ka zitukuko zimene akuchita mumadela osiyanasiyana mudziko lino. Mai Joyce Chitsulo MP akuti Boma Ndilomweli.
Mai Joyce Chitsulo MP akuti Mulungu adalitse Pulezidenti Chakwera ndipo amupatse moyo wautali kuti zitukuko zimene akupanga zipitilire patsogolo .