Joyce Chitsulo
Joyce Chitsulo
Hon Joyce Chitsulo
Mwanza West MP
Vote Now

MP ALIMBIKITSA CHIKHALIDWE CHA MAKOLO

None
Social Development

MP ALIMBIKITSA CHIKHALIDWE CHA MAKOLO

Phungu Wa kunyumba yamalamulo wadela la Mwanza West Constituency Hon Joyce Chitsulo lelo anali kudela lake komwe anakonza mpikisano wa madambwe a Gule wa Mkulu. Pa mkumanowu, Mfumu yaikulu Ntchache ndi Mfumu yaikulu Govati ndi omwe anali alendo olemekezeka kwambiri omwe unachitikira pabwalo la Thambani Community ground kwa Senior ChiefGovati.  

Mmau awo Mafumu wa ayamikira phungu yu pokonza mpikisanowu zomwe akuti siazinachitikenso mkale lonse komanso zapangitsa kulimbikitsa ubale pakati pa madera a Senior Chief Nthache ndi Senior Chief Govati.  

Pa mpikisanowu, dambwe la Senior Chief Nthache Headquarters ndi lomwe lagonjetsa onse ndipo lachoka ndi ndalama  zokwana  K300,000.00. Kamkoma Dambwe yochokera kwa Senior Chief Govati ndi yomwe yakhala yachiwiri ndipo yalandira K200,000.00  pamene Kagonamwake ya kwa Senior Chief Nthache yakhala yachitatu ndipo yalandira K100,000.000

Madambwe a Golowa, Mkwete, Tsegulani,  Machilika ndi Mandaawana achoka ndi K50,000.00 dambwe lililonse ya chipukuta misozi.  Chair wa Achewa ku Mwanza, Bambo Molosoni ayamikila phunguyu Pa chikonzerochi ndipo apempha Achewa onse aku Mwanza West Constituency kuti apitilize kugwira ntchito ndi Mai Joyce Chitsulo.