Mafumu amuboma la Mwanza, ayamikila mtsogoleri wadziko lino la Malawi 🇲🇼 His Excellency the State President Dr Lazarus McCarthy Chakwera powalemekeza mafumu komanso anthu a ku Mwanza. Mafumuwa amayankhula izi ku mwambo wolumbilitsa nduna ndi achiwiri kwa nduna za boma omwe angosankhidwa kumene.
Mafumu omwe ayankhula izi ndi a Senior Chief Nthache komanso a Senior Chief Govati aku Mwanza. Mafumuwa ati President Chakwera wawalemekeza posankha mwana waku Mwanza Mai Joyce Chitsulo MP kukhala Wachiwiri kwa Nduna Yowona zamaboma ang'ono ang'ono.
Senior Chief Govati komanso Senior Chief Nthache adapelekeza Mayi Joyce Chitsulo MP kumwambo wowalumbilitsa.