Wachiwiri kwa nduna ya maboma ang’ono, a Joyce Chitsulo, apempha makontalikitala am'Malawi amene akugwira ntchito zachitukuko zosiyanasiyana za boma kuti achite changu pogwira ntchitozi.
A Chitsulo anena izi m'boma la Ntchisi pamene amayendera ntchito zosiyanasiyana.
Zina mwa izo ndi yomanga police ya Malambo ndi Kaonga, zipinda zogonamo atsikana pa sukulu yondera ya sekondale ya Katete ndi zipinda zophunziriramo zapa sukulu ya pulayimare ya Champhoyo ndi chithandizo chandalama chochokera mu thumba la Governance to Enable Service Delivery ndi District Development Fund.
Koma, a Chitsulo ati ngakhale pali m'chitidwe ochedwetsa ntchitozi makontalikatalawa akumanga zinthu za pamwamba zimene zikulimbitsa mtima kuti boma linachita bwino kupereka mwayi kwa makotalikata achiMalawi.
Wapampando wa khonsolo ya ntchisi, a Marko Mphezi Mtengo, ayamikiraa boma poonetsetsa kuti ntchito ngati izi akugwira ndi aMalawi.
Iwo achenjezanso makontalikitawa kuti asabwezeretse masomphenya aboma m’mbuyo pomachedwetsa dala ntchitozi.